God is jealousy God is wroth
Kukonzekera Chisautso Chachikulu
Contact information, map and directions, contact form, opening hours, services, ratings, photos, videos and announcements from Kukonzekera Chisautso Chachikulu, Seventhday Living Spirit Ministries, Mangochi.
If the Nations persist in keeping Sunday instead of the Sabbath, and choose to obey the commandments of men not the commandments of God; and acknowledge man not God, or bow down to man not to God who created heaven, the sea and the springs of water, by keeping the commandments which are man's principles not of God; Shall the sun scotch with furvent great heat,, Rivers of water shall dry up and shrubs shall wither away and pastures shall be burned... For God is wroth of what is happening here on Earth...
Ndibwino kutaya mwayi wa maphunziro, ntchito kapena mwayi wokhala ndi chuma koposa kutaya mwayi wokalowa kunyumba ya phwando la Ukwati wa Mwanawankhosa
Gawo loyamba
Gulu Lopatulika limene liti likwanitse kupyola chisautso chachikulu likuyenera kukhala lopanda banga kapena chirema. Choncho, pamene chisautso chikuti chiyambe, Oyera mtima, amene asunga Malamulo a Mulungu ndi Chikhulupiriro cha Yesu, akuyenera kutsatira mfundo izi mu gawo loyamba:
1. Kuchotsa ulalikidwe wolalikira dzina la mpingo ndi kuyamba kulalikira Dzina la Yesu.
2. Kusiya kuwatembenuzira anthu ku mpingo ndi kuyamba kuwatembenuzira iwo kwa Khristu Yesu.
3. Kusiya kuwabatiza anthu mu dzina la atate, lamwana,ndi la mzimu woyera, ndi kuyamba kuwabatiza iwo mu Dzina la Yesu Khristu.
4. Kuchotsa malumbiro a paubatizo, paukwati, ngakhale malumbiro alionse mumpingo ndi kukana lumbiro lirilonse m'mabwalo a milandu.
5. Kuchotsa ubatizo wobwerezabwereza,ndi kukhazikitsa chiyeretso cha Mzimu chomwe ndi chofunikira kwambiri.
6. Kuchotsa mwambo wa m'gonero wa kawiri kawiri ndi kukhazikitsa M'gonero wa kamodzi pachaka.
7. Kuchotsa zifaniziro zilizonse za thambo la kumwamba, kapena za padziko kapena za m'madzi a nyanja yapansi mumpingo, monga: zoimiritsa ndi zojambulidwa pakachisi, pamabuku, pambendera, pansalu ndi pazovala zosiyanasiyana ndizo
✓ fano la mtanda
✓ diso la Satana
✓ fano la nkhunda
✓ fano la Angelo Atatu
✓ fano la dzuwa
✓ fano la mwezi
✓ fano la nyenyezi
✓ fano la malawi a moto
✓Obelisiki
8. Kuchotsa masewera a kuguba mumpingo,ndi kulimbikitsa magulu ophunzira Baibulo (Buku Lopatulika ndilo Mawu a Mulungu).
9. Kuchotsa mavalidwe a chisilikari, ndi kukhazikitsa mavalidwe olemekeza Mulungu ku magulu onse a mumpingo kuphatikizapo amayi, abambo, anyamata ndi atsikana.
10. Kuleka kuvala zovala zokhala ndi zizindikiro za Chipembedzo cha Mizimu.
11. Kuchotsa masewera a mpira mumpingo.
12. Kuleketsa kugulitsa kwa mabuku a Mulungu ndi kulengeza ufulu kwa anthu a Mulungu, womwe ndi ulere wa Mawu a Mulungu.
13. Kuchotsa utumiki wodzikuza wokhala ndi mayina a mwano, ndi kubwezeretsa utumiki wodzichepetsa umene sukhala nawo anthu otchedwa:
✓Atsogoleri
✓Rabi
✓Ambuye kapena
✓Atate
pansi pano.
14. Kuleketsa mapemphero opempherera anthu akufa, ndi kulimbikitsa mapemphero opempherera anthu amoyo.
15. Kuchotsa utumiki wa ndale, wofuna kukhala ndi maudindo apamwamba mumpingo, ndi kulimbikitsa utumiki wodzichepetsa.
16. Kusiya ntchito ya usilikari, imene imamkakamiza munthu kuweramira wolamulira.
17. Kuleketsa malumbiro a AY, mwambo woyatsa kandulo ndi zonyansa zilizonse mumpingo.(see next)
Click here to claim your Sponsored Listing.
Location
Website
Address
Mangochi