Uthman Al-Qasweer

Uthman Al-Qasweer

Share

Our aim is rejuvenation of tauheed and sunnah and killing shirk and bid'a

17/12/2024

Akazi akuzifanizira ndi azimuna 💔
Azimuna akuzifanizira ndi azikazi 💔
Makhalidwe abwino anaonongeka 💔
Swalah pano inasiidwa(anthu sakuiswali) 💔
Kusatira malamulo a Allah kunaiwalidwa 💔
Koma ola laimfa ndiloyandikira zedi kwaife 💔
Mizikiti mumakhala mulibilet anthu (empty) 💔
Ma stadium mukumazaza 💔
Zizindikiro zaqiyamah zikuoneka 💔
koma anthu sakufuna kusintha 😔💔

Oh Allah tikukupemphani mathero abwino
🤲🤲💓

07/12/2024

TAUHEED/AQEEDAH LESAON 4
LOADING IN SHAA ALLAH

02/12/2024

PHUNZIRO LA TAUHEED/AQEEDAH
LESSON # 3
pambuyo potchula zamitundu ya tauheed tatiyeni tifotokoze mwachidule kwambiri za mtundu ulionse paokhapaokha koma tiyambe ndi tauheed al rubúbiyah

1.Tauheed al rububiyah
kumenekot ndi kuvomeleza zot Allah ndiwayekha, ndiolenga chilichose chaziko lapansi komanso uye ndioyendesa kalikose, opereka moyo ndi imfa, odyesa.
ndipo kuvomeleza mtundu umenewu ndikwachibadwi ndithu ndipo simuzapeza mibado yapitayo k*ti imakanira za ntundu umenewu ayi, ngat mene wayakhulira Allah mu Qur'an kt
ولئن سألتهم من خلق السموات والارض ليقولن خلقهن العزيز العليم
mutat mwafuse kt kod ndindani amene adakenga kumwambi ndi nthaka azayakula kt amene adalenga ndi wamphamvu oziwa (Allah).
ndipo ma ayah onga awa alipo ambir mu Qur'an, mupeza kt Allah ak*tchula zama mushrikeenah k*ti amavomeleza k*ti Allah ndimwini kulenga, kupereka moyo ndi imfa, kudyesa ndizina zambiri, ndipo palibe amene adakanira zamtundu umenewu kungopatula kagulu kochepa chabe kawathu koma pansi oamtima akuvomeleza, kukanira kwao kumakhala chifukwa chozikweza.

timagulu tina topotoka mudini timakanira zoti ma mushrikeenah sanali kuvomeleza tauheed al rububiyah ngakhale pangono ndipo amaperekera umboni mayah monga awa
أفلا ينظرون إلي الإبل كيف خلقت والي السماء كيف رفعت والي الارض كيف سطحت
surah al qhashiyah: Kodi inu simungaone ngamila mene idalengedwera?, komanso kumwamba menee kudanyamulidwira(kukwezedwa), komanso men nthaka inayalidwira?
قَالَ مَنْ يُحْيِي الْعِظَامَ وَهِيَ رَمِيمٌ
adat kodi ndindan amene angaukise(angapereke moyo) mafupa ali ofumbwa?
وَقَالُوا مَا هِيَ إِلَّا حَيَاتُنَا الدُّنْيَا نَمُوتُ وَنَحْيَا وَمَا يُهْلِكُنَا إِلَّا الدَّهْرُ ۚ
ndipo adat palibeso umoyo wina kungopatula umen ife tiliwu tizafa komanso kukhala moyo, palibe chimene chimationonga ife kungapotula nthawi basi
فَقَالَ أَنَا رَبُّكُمُ الْأَعْلَىٰ
ndipo(pharaoh) adati ine ndimbuye wanu wapamwamba
ndima ayah ena amene iwowo amaperekera umboni
Alhamdulillah maulama adayakha kale iz ndipo tatiyeni tiziyakhe mwachidule kwambir koma momveka.

ma ayah amenewa akukamba zokukanira kwawo pankhani yakuukisidwa manda ndik*tiso akalipidwa ku akhirah, komanso akukana zoti palibe umoyo wina pambuyo paumoyo umene tiliwu, osat akukana zoti Allah ndiolenga, odyesa komanso opereka imfa iyayi.

k*ti muone ma ayah amu surat ghashiyah wo muona zoti Allah akuwafotokozera k*t aione ngamila komanso ndizina zimene atchulazo kt Allah anazilenga bwanji? ngat anakwanisa kuklenga zimenezo akakanike kupereka moyo kachikena? ndipo Allah anarchula zangamila chifukwa ndichinyama chimene chinali chachikulu chimene ma quraish(aluyah) amaweta anali nacho pafupi.

ndipo ma ayah amene akufotokoza za pharaoh sik*t iyeyo amakana ndi mtima onse ayi koma kunali kuzikweza pambuyo pot mtima umavomeleza ndithu, umboni wake ndikuyakhula kwa Allah koti
وَجَحَدُوا بِهَا وَاسْتَيْقَنَتْهَا أَنْفُسُهُمْ ظُلْمًا وَعُلُوًّا ۚ
ndipo adakana koma mitima yawo ili ndichisimikizo (ikuvomelez) ndithu, mopondereza komanso kuzikweza.

ndipo mukamvesesa zimene mupeza k*ti onse amene amakana za mtundu uwu kumakhala kuzikweza chabe km mitima yawo ikuvomeleza.

غايتنا إحياء التوحيد والسنة وإماتة الشرك والبدعة
kufikira ulendo wina tizafotokoze za mtundu wina in shaa Allah
kamng'ono kanu mchioembezo
Al-Qasweer Al salafiyy

27/11/2024

LESSON #3 LOADING IN SHAA ALLAH

27/11/2024

NDIZAPANGA TAUBAH MAWA

Ndipanga taubah mawa ndikuyamba moyo wanyuwani ndikadali nyamata moyo ndiwautali uwu, adagona ndipo sanazukeso......

M'bale wanga kachose mumtima mwako kumati ndikadali mnyamata ndizalapabe....
Ndangat achinyamata amene yatenga imfa asadamere imvi? 😭😭
Ndimimera ingat imene idaonongeka isanakololedwe? 😭😭😭
imfa imabwera mwazizi ndipo zintchito zabwino ndizimene zizak*thandize paziko pano ndi ku akhirah

25/11/2024

PHUNZIRO LA TAUHEED/AQEEDAH #2 pambuyo pokambirana za tathauzo la tauheed tatiyeni tipite kumitundu yake
Q: Kodi mitindu ya tauheed ilipo ingat?
A: Mitundu ya tauheed ilipo itatu 3
1.Tauheed rubùbiyah
2.Tauheed ulùùhiyah
3.Tauheed asmaà waswifàt
zindikiran k*ti pali timagulu topotoka muchipembezo timene timakana kugawa tauheed mitundu itatuyi ndipo amat kugawa tauheed mitundu itatuyi ndi bidàh chifukwa sizinapezeke mu Qur'an ndi sunnah kt tauheed ili magawo kapna k*ti mmitundu itatuyi...

chabwino funso likupita kwaiwo k*ti;: kodi kagawidwe koti zikakamizo za udhu zilipo 6 munazitenga k*ti? Mungatipase ayah kapena hadith imene yatchula kt zikakamizo za udhu zilipo 6?kpna nsichi za swalah zilipo 14?
ayi ndithu palibe amene angabwerese, naga funso mkumati zinatengedwa kuchokera k*ti?

izitu maulama amazitenga kuchokera mu maumboni omwewo amene akuoezeka mu Qur'an komanso mahadith pambuyo powasata bwino maumboniwo kt akukamba chani imene pachiluya amat(بعد تتبع الأدلة).

kotero maulama pambuyo powasata bwino maumboni ochokera mu Qur'an komanso mahadith anapeza kt mitundu ya tauheed ilipo itatu ngat mene adapezeraso kt zikakamizo za udhu zilipo 6,ndipo palibe amene angakane zimenezi kungopatula yekhayo amene mtima wake udapanga zimbiri ya bidah ndi shirk moti oil watauheed ndi sunnah ngakhale mutathira nawo mitima yawo siingafewebe kupatula Allah atafuna.

kotero palibe kunena k*ti kugawa tauheed magawo atatu ndi bidàh.

amene muli ndik*thekera kowerenga ndikumva arabic pali bukhu limene mungaonjezere ilm pankhani imeneyi lolembedwa ndi sheikh abdul razaaq badr, lalingono kwambir km lopindulisa lotchedwa:
القول السديد في الرد على من انكر تقسيم التوحيد

kufikira ulendo wina umene tizatambasule mtundu ulionse paokhapaokha ndikuyakha zosochera zonse zimene magulu opotoka amayakhula pamtundu ulionse in shaa Allah

ng'onoo wanu mchipembezo
✍️✍️Uthman Al Qasweer

غايتنا إحياء التوحيد والسنة وإماتة الشرك والبدعة

24/11/2024

PHUNZIRO LA TAUHEED/AQEEDAH
LESSON 2
LOADING IN SHAA ALLAH

21/11/2024

∆Phunziro lothandiza #
Al hasan Al baswar chisoni cha Allah chikhale pa iye adat:
Kuonongeka kwa mitima kumabadwa(kumachokera) muzinthu 6 📎📎
✓1.Kuchimwa muzina loti ndizapanga taubah
✓2.Kuphunzira dini ya Allah koma osaigwirisira ntchito
✓3.Akaigwirisira ntchito imakhala yopanda ikhlas
✓4.Kumadya ma rizq Allah koma osayamika
✓5.Osasangalasidwa ndi mmene Allah akugawira ma rizq ake kwa akapolo ake
✓6.Kumakaika maliro okha ndimanja awo koma osakhuzika mitima yawo

📕 #المصدر: إيقاظ أولي الهم العالية... 🌹

20/11/2024

PHUNZIRO LA TAUHEED/AQEEDAH PART 1

Q: Kodi tauheed ndichani?
A: liwu lot tauheed pachiluya mphata lake ndi
وحد، يوحد، توحيدا
k*tathauza k*ti kuchiika chinthu pachokha
pmene pa shariah akat tauheed amatathauza: kukhulupilira kwa kapolo k*ti Allah ndi modzi pa iye yekha komanso wayekha pamayina ake ndimuzichitochito zake ndipo palibe ophatikizana naye muchilichise muzimenezi, ndipo k*ti Allah ndioyeresedwa muchilichise chimene chili chopunguka komanso chilichose chimene chili ndivuto mkati mwake(mbiri ilionse) limozi ndikumpatula Allah paibadah ilionse.

mutathauzo limenelo mupeza k*ti Allah ayenera kupatulidwa mwa iye yekha, mayina ndimbiri zake komanso mu umbuye wake zimene zili zichitochito zake, imene ili mitundu ya tauheed yo...
Q: Nanga liwu la tauheed ndilit?
A: liwu la tauheed ndi
لا إله إلا الله
Lailaha illah llah
k*tathauza k*ti palibe mulungu wina opembezedwa mwachoonadi kupatula Allah
ndipi liwu limeneli silingakhake lofunikira kungopatula ndi zinthu
awiri basi k*ti likhale lokwabira
نفي وإثبات
kulesa kapena k*ti kukana ndikusimikiza basi
لا إله(نفي)
mawu oti palibe mulungu ndikukana(kulesa)
إلا الله (إثبات)
pamene liwu loti kupatula Allah ndikuvomeleza kapena k*ti k*tsimikiza ndik*tsindika...
mukatero liwulo likhala lofunikira
komanso lili ndi malamaulo ake k*ti likhale lokwanira bwinobwino tizakambabe in shaa Allah...
Q: Kod aqeedah ifeo asilamu timaitenga k*ti?
A: Aqeedah yolondola timaitenga kuchokera mu Qur'an komanso ma hadeeth a swaheeh ndizimene ummah udagwirizana(إجماع).
Note: osat ijimah iyi ya anthu wamba ai komano tikukamba za anthu amene adachemeleredwa ndi mtumiki ndikuyelesedwa.
ndipo asatinamize k*ti nzeru zathu zili ndi gawo pa aqeedah ili ndiboza ndithu

to be continued..

20/11/2024

KODITU MKAZI SAIPA CHIFUKWA CHAUMPHAWI NDI MAONEKEDWE, MKAZI AMAIPA KAMBA KA LILIME LAKE NDI KHALIDWE LAKE

19/11/2024

nkhani siili kungokhala salafiyyah zina lokha ma socil media mu basi.. 📱💻
khalani salafiyah pa ibadah yanu #
pamakhalidwe anu ndi bambo ndi mayi anu ♥💕'salafiyah pakatsatiridwe ka mtumiki wanu, salafiyah ndi azibale anu, azikazianu, amuna anu, ana anu, salafiyah ndi azinzanu, mudzi wanu...
salafiyah pakugamula zinthu zanu, komanso salafiyah mudziko lako lonse osati pongozipasa mayina oziitanira k*ti salafiyah pa Twitter, Facebook, instagram and any kind of social media.

salafiyah ndi njira imene mumasata paumoyo wanu ndipo salafiyah nde umoyo umenewo

19/11/2024

"Machimo ndi chain chimene chimakhala mukhosi la ochita tchimolo ndipo sichimavuka mkhosimo kungopatula ndi kupepha chikhululuko kwa Allah ndikulapa"
Ibn jauzi

let's get addicted to istighfaar we sin alot

Want your school to be the top-listed School/college in Salima?

Click here to claim your Sponsored Listing.

Location

Category

Telephone

Website

Address

Salima