Whoever has lost their Lord in their heart,
How can they ever taste the sweetness of faith?
Alll desires may be attained with wealth,
Except the final destination to the abode of grace.
من كان يفقِدُ ربّه في قلبهِ
أنّى يذوقُ حلاوةَ الإيـمانِ
كلُّ المطالب قد تُنالُ بدرهمٍ
إلا المصيرَ لمنزل الإحسانِ
Al Iman Wal Istiqama
An Islamic page with authentic narrations
UBWINO WAKUSALA MASIKU ATATU APAMWEZI
Uku ndikusala masiku atatu mwezi ulionse ndipo masiku abwino ndiwo pa 13,14 ndipa 15 mondondozana. Kusala uku Mtumiki adakulimbitsa pakati pamaswahaba ake ngati mmene zafikira muhadith yamu Bukhar ndi Muslim kuti Abu Huraira adalangizidwa kuti asadzaphonye kuchita zinthu zitatu kufikira imfa yake:Kuswali Witri usiku ulionse, kuswali swala Dhuhaa kummawa kulikonse komanso Kusala kudya masiku atatu apamwezi mmwezi ulionse. Komanso mmene zafikira mu Bukhar ndi Muslim muhadith imene adalongosola Abdullah bun Amru bun Al Aasw kuti Mtumiki adamuuza kuti Kusala masiku atatu apamwezi azilandira Malipiro kuchulukitsa ka khumi pantchito iliyonse choncho Kusala masiku atatu zifanana ndikusala mwezi onse. Muhadith ya Abu Dharri yomwe ikupezeka mu Tirmidh ndi Nnasaai ndipo Imam Tirmidh adati ndi Hadith ya Hasan ndipo adagwirizana nazo Imam Alban kuti ndiyahasan, Mtumiki adamuuza Abu Dharri kuti Ukafuna Kusala ndibwino uzisala masiku atatu apamwezi.
Kusalaku sikunaikidwe masiku enieni okakamizika, utha Kusala kumayambiliro kapena kumapeto koma zabwino zake ndizo Kusala masiku apakati omwe ndi 13,14 ndi 15 mmwezi wakumwamba(Hijri). Choncho tafuna kukumbutsana kuti mwezi uno masikuwa akulumikizana ndipa 16,17 mpaka pa 18 October lomwe ndilachitatu, lachinayi ndilachisanu. Zichitikanso ubwino kuti kwa osala lolemba ndilachinayi, lachinayi pa 17 uzakhala double chifukwa Niya ya double pakusala ngati uku ndizololedwa. Iyi ndiSunnah yabwino kwambiri yosafunika kuiphonya. Baarakallah fiikum
Mu Hadith ya Abu Huraira Rawah Imam Ahmad komanso Ibn Hibban yomwe Shaikh Alban ataifufuza adati ndiyaswahih, Anthu ena adati kwa Mtumiki 'Oh Inu Mtumiki, mzimai wina amaswali usiku onse swala zausiku ndipo masana amakhalira Kusala kudya, koma lirime lake limakhalira kunena zoipa za aneba ake.' Mtumiki adati IYEYO NDIWAKUMOTO. Ndipo anthuwo adati 'Ndiye Pali mkazi wina, amangoswali swala zokakamiza zija basi ndipo masana samasala kudya, koma lirime lake samakamba zoipa zaneba wake' Mtumiki adati IYEYO AKALOWA KUJANNAH.
Nkhani iyi ndiyoopsa kwambiri, tichenjere!! Kukhalira kukamba zobisika zaena, kufooka kwaena, kukhalira kukamba za anthu ena ndichinthu choletsedwa ndipo ndichinthu chomwe chikalowetse anthu ambiri kumoto. Mukukamba kwa Mtumiki madalitso ndi Mtendere zipite kwaiye adati ambiri akalowetsedwa kumoto chifukwa chalirime ndi maliseche awo.
Tsiku Lina Mtumiki adamuuza Muadh kuti SAMALA NDI LIRIME LAKO. Muadh adati 'Kodi tikafunsidwa pazomwe lirime limakamba Inu Mtumiki?' Mtumiki adati NDICHANI CHOMWE AMBIRI AKALOWERE KUMOTO AKUKHWEKHWEREZEDWA NKHOPE KAPENA MPHUNO ZAWO PANSI KUPOSA ZOKOLORA ZAMA LIRIME AWO?? A serious matter wallah! Intabih!!
Muhadith imene tsinde lake ndi Imam Bukhar komanso Muslim yomwe adaitulutsa Imam Tirmidh, Ahmad komanso Ibn Majah kuchokera kwa Abu Huraira ndipo Shaikh Alban adati ndi Hadith yoonadi, Mtumiki adati MUNTHU AKHONZA KUYANKHULA MAU, MAUWO NDIKUMUKWIITSA ALLAH NDIPO AKAMULOWETSA KUMOTO. ZIKATENGA ZAKA 70 ASADAFIKE PANSI PAMOTO. Pankhani zanzanu, samalani. Pankhani zaneba wanu, samalani. Mind your own business as much as you can, zimenezo ndizabwino kwainu kuposa kukometsa macheza pankhani zawina
Allah azititalikitsa kumchitidwe okamba zaena nthawi zonse!!
TAURIYAH.
Kumeneko ndiko kunena mau atanthauzo limodzi kwa okumva koma oyankhulayo akudziwa matanthauzo awiri ndipo akutanthauza tanthauzo lina losiyana ndilomwe wakumva wamva.
Ndipereke Chitsanzo pachiyankhulo:
Munthu atanena kuti ndilibe olo 1tambala zimasonyeza kuti alibe ndalama,koma pa TAURIYA atha kunena choncho akufuna kutanthauza kuti 'ndilibe 1tambala yasilver(yosintha)' koma mthumba ali ndi 100kwacha yapepala.
IMAM NAWAWI adanena kuti anthu ophunzira adaika lamulo la TAURIYA ponena kuti Ngati ukufuna kuteteza lamulo lashariya kapena kuteteza munthu kapena kuziteteza utha kugwiritsa ntchito. Muhadith yopezeka mu SUNAN ABI DAUD kuchokera kwa AISHA iye adanena kuti MTUMIKI ADATI 'AMENE UNGADUKE UDHU WAKE ALI PASWALA YAPAGULU AGWIRE MPHUNO ZAKE KENAKO ACHOKE PASWALAPO.' Pamenepa Mtumiki amafuna kutsindika kuti UDHU UKADUKA upite ukapangenso wina,koma zimenezi zitha kuoneka zochititsa manyazi chifukwa apa ndipagulu,Ndiye Mtumiki adaikamo mau oti AGWIRE MPHUNO ZAKE ndicholinga choti anthu azimuona ngati akupanga kamfuno ndiye watulutsa magazi ofunika akapangenso udhu.Ndipo uku sikunama koma kuti KUGWIRITSA NTCHITO ACTION YOMWE ANTHU AZIONA TANTHAUZO LODZIWIKA POMWE OCHITAYO AKUDZIWA TANTHAUZO LOBISIKA. Chitsanzo china ndichomwe IMAAM IBN AL QAYYIM adachilemba mubukhu lawo la IGHAATHAT AL LAHFAAN kunena kuti Hammad adali ndimchitidwe oti akafuna kuti asacheze ndimunthu amanamizira kukuwa MAINE DZINO LANGA!!! MAINE DZINO LANGA!!! ndiye yemwe wabwera kuzacheza naye uja amati iiiii sinanga shaikh akudwala nkutsanzika. Imeneyonso ndi TAURIYAH pofuna kum***amangitsa munthuyo yemwe samafuna kucheza naye koma mwaulemu, Imeneyonso ndi TAURIYA.Zimenezi m***a kuzipenzanso mmabukhu monga Ighaathat Al Lahfan Ya Ibn Qayyim Komanso Al Adab Al Shariya Ya Ibn Muhfin.
MADZULO ABWINO!
ANTHU OMWE ADASANDUTSIDWA ANYANI
Allah mu Surat Maida ndime 78 akulongosola kuti ANATEMBELEREDWA ANTHU AMENE ANAKANIRA OCHOKERA MWA ANA A ISRAEL PALIRIME LA DAUD KOMANSO ISA MWANA WA MARIUM, ZINALI CHONCHO CHIFUKWA CHAKUNYOZERA KWAO KOMANSO KUDUMPHA MALIRE. Anthu amene adatembeleredwa palirime la Daud ndiomwe adachita makani tsiku loweruka. Anthu amenewa adapatsidwa lamulo kuti asamasoze(asamapite kunyanja) tsiku loweruka. Tsiku limeneli lidaikidwa kukhala lopatulika kwaiwo. Ndiye Allah adafuna kuwayesa mayeso, nsomba zija zimasowa kuyambira lolemba mpaka lachisanu, akafuna kuweza samapeza kalikonse. Likafika loweruka(lomwe analetsedwa kuwezalo) nsomba zija zimaonekera paliponse, zimachita kuyandama pamwamba pamadzi. Likafika lamulungu nsomba zija osaonekanso zimazaonekanso loweruka linalo. Anthu aja anapanga plan, anayamba kutchela nsomba zija lachisanu kuti zikodwe loweruka ndikukavuula lamulungu. Kenako anatailira mpaka adayamba kuweza loweruka loletsedwalo. Allah akulongosola mu Surat Aaraf:
Tawafunsani nkhani ya
mudzi umene Udali m'mphepete mwa nyanja(Anthu
Am'mudziwo) pamene adali kuswa (Lamulo la)tsiku la Sabata,Nsomba Zawo
zinkawadzera yandayanda Patsiku
la Sabata, koma patsiku Lomwe silidali la Sabata sizidali yandayanda.Pamene anadzikweza
Pakusasiya zimene Analetsedwazo
tidawauza: "KHALANI ANYANI ONYOZEKA."
Anyani amenewa adali munthawi ya Mtumiki Daud kalekale kwambiri Mtumiki Sulaiman ali wachichepere kapena asanabadwe kumene. Iwowa adali pamalo otchedwa ILYA pafupi ndiphiri la TURI ku MEDIAN komwe masiku athu ano kukutchedwa ku JORDAN. Anyaniwa sanabelekane chifukwa chidali chilango pazomwe iwowo adachita. Ndipo atatha kumwalira, kagulu ka anyani amenewo kanathera pompo. Awa tikuwaona lerowa siomwe adasandutsidwa munthawi ya Daud ayi. Allah munkhani zawo akulongosola mundime 65 yamuSurat Baqara kuti NDITHU MWAWAZINDIKIRA AMENE ANACHIMWA TSIKU LASABATA NDIPO TIDATI KWAIWO KHALANI ANYANI ONYOZEKA.
Munkhani imeneyi muli malesson angapo, Allah akabweretsa lamulo sitimafunika kuchuluka nzeru koma kutsatira chifukwa ukachuluka maplan palamulo la Allah, mapeto ake ndichilango chopweteka. Anyaniwa siomwe tikuwaonawa, tikuwaonawa ndimtundu weniweni wa anyani olengedwa pachiyambi chachilengedwe..
Kodi amene adasandutsidwa nkhumba adalakwa chani? kodi nkhumbazo zikadalipobe? Iyi ndinkhani yathu yamawa INSHALLAH ine Mng'ono wanu mwa Allah Abdulhasiib Mainas ndikufunirani Tsiku lopambana!
Click here to claim your Sponsored Listing.
Location
Category
Contact the school
Telephone
Website
Address
Mangochi