Chikondi chathu stores

Chikondi chathu stores

Share

We write οΏ½ and romantic stories , which might improve people's relatuonships

23/09/2022

Hi g**z mwandisowa eti.....osadanda pompan ndikhara ndikuyamba chinkhani chokoma kwabasi.

02/03/2022

BWADZI LOKONDA
πŸ‘‡πŸ‘‡πŸ‘‡πŸ‘‡πŸ‘‡πŸ‘‡πŸ‘‡πŸ‘‡πŸ‘‡πŸ‘‡πŸ‘‡
Eeee koma dziko likundida chonchi bwanji? Mayi kumandako munandisiranji ine kuti ndizidzuzika chonchi? Ngati Kumwamba kuri Mulungu nakha bwanji simukundisithira moyo wanga, chifukwa chani munatenga makoro anga ose kundisiya ndekha ooooh Mulungu wanga!!!! Ukutu kunari kudandawura kwa nyamata wina otchedwa kenneth komwe uko ku Chiladzuru......

Bwanji ken ukungodandaru chotere?
Gibo ndisakunamidze nyengo zomwe ndikudutsa ineyo kwabwino ndingifa basi chifukwa dziko landilaka iri.
"" Mzanga osamatero ndiripo ine ndipo nyengo dzomwe ukudutsadzo zidzatha, ndipo athu omwe akukudzudza lerowa adzakugwadira ndithu.
"" Mmmm siya kulotako Gigo zotsatheka zomwe ukukambadzo, athu oti akudyelera chuma chamakoro anga..
"" Zitaye zimenedzo tiye kudimba tikadye magwafa mwina kumayiwarako mavuto.
________________
Kodi chisiru chija chapitatso kuti ndikufuna chindichapire dzovara dzangadzi?
"" Matia ukunena kenneth, khangati wapita kodyetsa mbudzitu.
""" Ndiye mpaka nthawi zino sanabwere adya ndowe zambudzi lero ndithu akuwona ngati ndine mayi wake eti.
""" Ndipo Amayi ndikawuletse kuchipinda kwangaso sanakolope lero.
"" Osadandaura kathy aziwona lero ameneyo ndipo awakumbukira makoro ake ndithu.......Awatu ndi azakhari anga umwe ananditenga after amokoro anga kumwalira payimfa yagalimoto, Ndiye si nkhadza zake zomwe ndimapandira pakuti ntchito zonse zimayang'ana ineyo Ana awo matias ndi kathy amangokhara ndipo samva oro ndichisone chomwe.

_______________
Eeeee koma kupanda iweyo gibo sindikuxiwa ngati ndikanakhara ndimoyo ayi chifukwa chimwalirilen makoro anga ndikungotutsa muzilango basi.
"" Osadaanda iwe ndikamakuwone ndimakutenga ngati m'bare wanga chifukwa oro makoro ako anari moyo sumawonetsa mtima ozikonda ayi, ndipo chilichotse tizipangira limodzi ngati brother wanga.
""Oooh ndikulephera kuti ndingathokudze bwanji chifukwa kubanja lakwanu konse mumandiwonesera chikondi chopambana,,β€’β€’β€’β€’β€’β€’β€’TAYAMBA CHONCHOTU

20/11/2021

ZOKHUMBA ZA MUTHU
γ€°γ€°γ€°γ€°γ€°γ€°γ€°γ€°γ€°γ€°γ€°γ€°γ€°γ€°
Kathy ndimakukonda chonde usapite? Usandinyase garu ngati iwe ungandipatse chani ndipo kaya ndinakulolera mankhwara sindikudzi, pita ukasake akamadadza adzoko oti azikhalira kudya dairy osati ine ayi..Kathy ukuyakhura ndiweyo zimenedzo................ikhara ikufika posachedwa ingotini pheee, NDIKATERO NDIMAKHARA NDAFIKA

16/10/2021

Monday mukhare okonzeka chifukwa ndikuyambapo kulemba nkhani, nditasowa kwakanthawi.....koma izikhara yayifupi chifikwa ndilembera kuzera pa liteπŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯

11/09/2021

Morning morning nonse muno? Ndikuziwa kuti nkhani mwazisowa pano, vuto ndilomwelija, muthune ndayesetsa umandiumu koma sizikutheka.....ndiye vuto la Facebook lite amachita kukupatsa malire ndiye nkhani yake imakhara tayifupi, ndiye ndizilembera lite yomweyi? Chifukwa ma apple omwe ndimagwilitsa ntchito akukana????

04/09/2021

WAWA OWELENGA NONSE MUNO, MWINA MUKUDABWA KUTI KWANGOTI ZII BWANJI, Nkhani ndiyakuti Facebook yemwe ndimalembera nkhani panopa sakutheka, ndikasegura kuti ndilembe nkhani zikukanika ndithu. Ndiye zikatheka muwona ndibwelatso koma pakanthawi kameneka ndidikireni ndithu. Vuto lonseri labwera chifukwa cha free data............

26/08/2021

UMASIYE KUWAWA
PART 9
😫😫😫😫😫😫😫😫😫😫😫😫😫😫😫😫😫😫😫😫😫😫😫😫😫😫
Mr Gama atafika pakhomo anapedzadi Akadzi awo atapita, koma kuti panthawi palibe chomwe chimayenda ayi....Miyedzi ingapo inadutsa ndipo Mr Gama chifukwa chamavuto aynayamba kuwotcha makara kuti mwina zithu zingasithe koma palibe chomwe anapindura...
Oooh Ambuye ndikuziwa ndinakuchimwira komaso ndinachimwirapa pansi pano koma chonde musandiwumire mtima ndipatseni mwayi wina,,,,,ukutu kunari kulira kwa Agama kupephe chikhululukiro kwa Mulungu,,,,,,Ngati ukufuna ntendere ukuyenera kumufunafuna mwana wa chemwari wako ndikupepha chikhulukiliro,,,,,Oooh koma maloto amenewa akutathauzanji? Ndiyekutidi minyama yonseyi inachokera pa mwanauja eti. Basi mawa ndikuyenera kupita kwa gurupa akandithandidze.,,,,,,

""Sono katunduyi bwanji?
""Osamangoyang'ana bwanji, akupita nyumba mwako?
""Iiii basi zatha, ine ndakufutsani mwachulungamo inu ndipamene mukuyakha zosakhara bwino. Mumawona ngati zimwe mumachitadzo sizidzawulurika?
""Mirriam wafika pondiyakhura ine zimenedzo, koma ukuziwa kuti ndine amene ndinakubara?
""Munandibara ineyo, osati munachita kunditora pathengo iyayi? Chifukwa mukanakhara kuti mumaziwa kupweteka kukwakubereka sibwedzi mukumuchita nkhadzi Ken mpaka kum***amangitsa.""Kwakwana kwasara ulirapo apa,,,,,, Kodi chikuchitika ndichani apapa, nakha inu mwabwera nthawi zanji?
""Muchifutse chizukuru chanucho."""sona zitutuwelidzi bwanji?
""Nanu mungokhara chete sindinafikire panyumba panu koma panyumba panga."""He he uziwona ndikuziwa kuti banja ratha chifukwa chakharidwe lako, apa ndiye ubwire Masamba uwuziwe moyo,,,,,,,masiku ndiye amathera kuchiseko ndipo mayiyu palibe chomwe chimayenda ndipo anangoyamba moyo ogonana ndi azimuna kuti azipedza thandidzo.

"""Hi Nyamata paja dzina lako ndani?"""Ndene Kenneth sir,,,,Ok wandipasa chidwi kwambiri maka pakulimbikira kwako.
""Zikomo kwambiri sir kamba kakuyamikira kwanu."""koma ndimafuna ndikupepepheko pang'ono?
""Ok sir, m***a kutero ndithu.
""Ndimati masana ukaweluka uzikagwira ganyu pa company panga?
""Sir palibe angakane Mwayi umenewo, koma ndintchito yanji?
""Kodi paja kuno ukupanga za Acoutant eti?
""Eye sir ndichoncho.""Ok ndikufuna uzikhawelengetsa ndalama zomwe atha agulitsa siku limenero, zitheka eti?"""Eya zitheka sir,,,,,,,Ken ganyu ndiye anayiyamba ndithu, ndipo amati akaweluka amapita kuganyu ndipo zimamuyendera bwino kwambiri, komaso bwanayi amamukonda chifukwa zithu amazilondolidze bwino,,,,, Ken ndisaname wandipatsa chidwi kwambiri, ukuzalemba mayeso ndikufuna uzakhare konkuno uzizayendetsa company ino?
""Zikomo kwambiri sir, koma pankhani mwanenayo mundipatse Kaye mpata ndiganidze bwino."""Ok uzadzakonzeka uzandiwudza coz malo ako alipo kare ,,,,,,,,,,,,

""Wawa Mfumu yanga?
""Eeee!! Fikani gwadirani pachikumbapo.""Zikomo Mfumu.
""Kaya mwaswera bwanji Agama?
""Inetu ndaswera bwino sindiziwa inu Mfumu?
""Ineso ndaswera, Kaya tikuwopeni?
""Inetu musandiwope kwenikweni, Choyamba ndafuna ndipepetse pazomwe ndinachita pazana, pasakuyakurani bwino,,,,,,,,,Ndakumvani, ndiye mukufuna ndikuthandizeni chani?
""Mfumu ineyo pano zithu siziritso mwakare pakuti palibe chomwe chikuyenda, ndiye nditawyngudzawungudza zapezeka kuti nkhani ndi Ken, ndiye ndimafuna mundithansidze kuti ndimupedze,
""Mmmm ok, koma mukuziwa kuti kwapita zaka zingati?""Eye zitha kukhara mwina dzaka khumi pano.
""Ok koma mumakumbukira mawu omwe munayakhura pano?
""Pepani kwambiri Mfumu ndikhulukilireni pachimenechi.
""Ndiye ndikuwudze komwe kuri eyi pano sindikuziwa komwe ari, ndiye utha kunywmuka muthu opanda zeru iwe.
""Chonde Mfumu ndithandizeni ndimupedze chifukwa iyeyo ndiye chiyembekedzo changa.""Waziwa lero zimenedzo eti? Ndiye ukuyenera kupanga wekha zimenedzi osati ine ayi.........

""Kumbari ya Mayi ake a Yobu ndiye anayamba kudwara ndipo analephera kupita mwasing'anga koma palibe chomwe chimasitha, ndipo siku lina anapita kumapephero kuti mwina akapedze chithandidzo, Uku ndiye anawauza kuti akuyenera kumupepetsa mwana yemwe anam***amangitsa pakhomo pawo chifukwa Mulungu anakwiya nanu kwambiri...
Mwawonatu Amayi inu mumawona ngati mukuchenjera lero ndi idzi mizimu yakukathani, akakhara Yobu ndiye ndiwuyo akulikundendeyo.
""Mummm mummm, Chonde mwana wanga ndithandize kumupedza Ken?
""Ndikupezera kuti ineyo sono, popedza kuno anasamuka kalekare?
Mummm Mummmm,,,,,,,,,

""Sir ngati mungandilore ndikuyenera kupita Kaye kumudzi ndikawone athu,,,,,,Apatu kuti Ken atasara ndi chaka chimodzi kuti amalidze, Mulungu akalemba palibe angafufute, tangoganizani ukuphudzira kwinaku ukuphatso ndalama.,,,,,,Ok panga zimenedzo, koma uziwe kuti ukazabwera udindo wako ndo u Co wacampany ino.
""Zikomo sir,,,,,,Masiku ndiye amathamanga mpaka siku loti Ken alandire degree yake linakwana, ndipo kunari mwambo wabwino kwambiri pakuti Ken chomwe amafuna chinatheka,,,,Oooh Mirriam, ndikuyenera ndikakafika kunyumba ndikapita kumudzi ndikamuwone Chemwari wanga ndamusowa kwambiri, beib komaso uncle ine ken ndikubwera kumudzi koma ndiri ndichuma pakuti Mulungu wandipambanitsa,,,,,,,Siku lobwelera kumudzi linakwana ndipo Ken anasazikana ndi azimzake komaso sir ake omwe anamuwudza kuti akazakomzeka azawawudze.,,,,,,,,,,Kodi idzi zitha bwanji maka Ken akafika kumudzi kuno????? Kalani pomwepa ndikudikira mwatcheru kuti mawa kubaranji...OSAYIWARA KUPANGA COMENT KUTI NKHANI IBWERE MWACHIKOKA.

Pangani like page ino kuti nkhani zidzikupezani mosavuta.

25/08/2021

UMASIYE KUWAWA
PART 8
😫😫😫😫😫😫😫😫😫😫😫😫😫😫😫😫😫😫😫😫😫😫😫😫
Mu part saven tinalekedza pamene Kenneth amapita kwachibwedzi ckake. kwinaku Mr Gama ayamba kuzindikira pakulakwa kwawo.
πŸ‘‡πŸ‘‡πŸ‘‡πŸ‘‡πŸ‘‡πŸ‘‡πŸ‘‡πŸ‘‡πŸ‘‡πŸ‘‡πŸ‘‡πŸ‘‡πŸ‘‡πŸ‘‡πŸ‘‡πŸ‘‡πŸ‘‡πŸ‘‡πŸ‘‡πŸ‘‡πŸ‘‡πŸ‘‡πŸ‘‡πŸ‘‡
Tinanyamuka ngati masewera ndithu, Beib ndiye wati makoro ako unawaudza za ine?
""Ken ineyo ndimakukonda ndipo ndinachiwona chanzeru kuti ndiwawudze makoro anga za iweyo.
""Oooh Moureen iwedi ndipatari and I hope kuti makoro akowo akasangalasidwa nane eti?
""Ndipo usakayike mix ndinawawonetsa kare zithudzi dzako.,,,,,tinsyenda ndipo mwakanrhawi kochepa tibafika pa nyumba ya makoro ake a bwedzi langari,,,,,,,,yeah tafika sopano tiyeko tilowe?
"""Oooh ok chabwino,,,ngakhare ndimalowa komabe ndinari nditimatha pang'ono nokhaso mukudziwa muthu akamapita kuchipongodzi simatha akewo tosakanidza ndimanyadzi wez.

""Ndakulandira mwana wanga
""Zikomo Amayi,,"""Tiyeni tilowe nyumba kuti tikachedze bwino,,,,Ok, ndiye Adad alikuti?
""Alipo kungoti alowa town koma sakachedwako,,,,Waswera bwanji nyamata?
""Ndaswera kaya inu Amayi?
""Ndaswelatso bwino ndithu,,,ndikukhulupira kuti inu ndiye Apongodzi eti?
""Eya ndichoncho ndithu"""""Ooh nkhani yabwino ndakulandira ndithu pakhomo pano.""Zikomo Amayi,,,,,,, Amayi ichi ndiye chiphona changa chomwe chaponda Ana a school onse iye ndikubwera pa top.
""Ooh zosangalatsa kwambiri, ukuyenera kulimbikira kuti khumbo lako likwanilitsidwe basi.
""Ndiyesetsa ndithu Ama,,,,,,, Tiri mkati mochedza bambo wapanyumbapa anatulukira koma manja mwake atanyamura chikwama ndithu koma ndizoti anari atachikutulira moti muthu ndipovuta kuziwa kuti muri chani.

""Pongodzi wanga alikuti kodi?
""Adad osatipatsa Kaye moni bwanji?"""Aaa inu ndimakuwonani dairy ndiye chokupasirani moni ndichani?
""Komatu achoka ndipo mutifuna ndithu.
"kkkkkk, Nyamata waswera bwanji?
""Ndaswera bwino kaya inu Madara?
""Aaaa ineso ndaswera,,,,,I hope suzamukhumudwitsa mwana wanga eti?
""Yeah, tachokera kutari ndipo ndikhumbo langa kuzakhara naye ndithu.
""Oooh ok, ndakulandira kunyumba ino ndipo ukhare omasuka osamawopa ukafuna kubwera?
"""Zikomo kwambiri,,,,,,,,Tinachedza ndithu kwakanthawi kenako thawi yoti ndinyamuke inakwana,,,,Amama komaso Madara ndimafuna ndikuthawenitu?
""Oooh, osagona komkuno bwanji?
'""Aaaa paja ulendo wanga wasara pang'ono ndiye ndikuyenera kupita kuti ndikamve momwe zikuyendera.
""Ok ndiye ndiye tadikira ndikupatse mphotso yako yonwe ndinakukomzera,,,,,,Ananyamuka kulowa kuchipinda komwe anabwera ndichikwama chomwe ndinachiwona chija.
""Ngakhare iri yochepa koma landira ndithu.
""Zikoma Madara chifikwa champhotso imeneyi ndipo Mulungu oziwa kudalitsa akudaliseni.,,,,,Ndinasazikana ndi makoro ake a Moureen kenako tinatuluka,,,,,,Beib sindimayembekezera kuti makoro ako angandilandire choncho.
""Ndinaziwa ine kuti unari ndimatha kkkkkkk.""Beib koma ndikupepha kuti pomwe tikusiyana mwakanyengo ndikupepha kuti uzisamalire?
""Ken ndimakukonda ndipo uziwe kuti ulipo wekha yemwe ndinasakha, ndizidikira iweyo basi.
""Ok ndakumvani dear,,,,,,,,

""Masiku ndiye amapita mpaka tsiku lonyamuka Ken kupita Ku UK linakwana,,,,,,Phwanga ukupitako ndikuchilendo ndipo zochitika zake ndizosiyana ndikuno, ukuyenera kuzidziwa kuti ndiwe ndani nakha ukupita kumeneko kokatani. I hope suzandikhumudwitsa?
""Uncle musadandaure, chomwe ndikufuna ndikuzimaludza zimenedzi kuti athu azachiti wokho manyadzi.,,,Mwana wamzeru , komaso uzikumbukira kuti wasiya mthiti yakoyi kkkkkkk!!,
""Amenewa akuziwatso momwe ndimawakondera ndipo sindingawasiye mophweke ayi.
""Ok nthawi yakwana yoti unyamuke ndiye sadzikanani mwabwino ndi madam anuwo.

""Moureen chonde uzisamalire wekha, chiyembekedzo changa ndiweyo?
""Osadanda uzandipedza ine, ndipo ndizidikilira iweyo.,,,,,Tinahaga kenako ndinapita kukakwera ndege. ukutu kunari kuyisiya mthaka yamalawi..........

"""Lero mwadzindikirano kuti mumachita Zolakwika eti?
""Chisare wekha ukuwonaso ntchito anandichotsa, mkadzi wanga angondipangira mwano okhaokha.
""Aaa Gama inetu ndimanena koma iwe umawona ngati ndikuyakhura zisakhara bwino, Ndiye bwanji upite kwa Chimwara emwe umayenda naye uja?
""Mmmm musandipange choncho bro ndithandizeni?
""Ngati ukufuna kuti iweyo ukharebe mzanga ukuyenera umupedze mwana wanchewari wako kaye.
""Ndiyambiri pati kumusaka m'mene ndinamunyodzera kwa Gurupa kuja, komaso ndinamva kuti phunzitsi uja anasamuka kudera kuno.
""Ukamamva kuti midzimu yakwiya ndiye ndizimenedzi.
""Ok basi ndipita ndiwona kuti nditani.,,,,,Mr Gama ananyamuka kumapita kunyumba kwawo, Ndiye kaya ndimwayi kaya soka atafika kunyumba kwawo anangofikira kukakha chiseko kulowa nyumbamo koma zomwe maso awo anawo sanathe kukhulupilira ayi. Anapedza akadzi awo akubulira ndikukoma chifukwa panthawiyi nkuti atachiyita na chibwidzi chowo paganidza kuti amuna awo abwera madzuro,,,,,,,Ma Yobu kana ndizimene mumapanga ine ndikachoka eti?
""He ha he ha, sizimene mukuganizadzo ayi, chonde ndikhulurukilireni?
""Osadandaura ubwino wake uri ndikwanu ndiye chomwe uchite utenge katundu wako komaso ndiamunakowo muzipita ndisanapange ngodzi. ndikamamwebwera uku ndipedze mutachoka osayiwara kutengaso zovara za chiwanda chako chija.,,,,Mr Gama abaturuka nyumbamu koma osakuvetse zomwe achita akadzi awo maka akaganidza kuti amapanga chilichonse kuti azisangalara pakhomopo,,,,,Oooh apa ndiye yakwiyadi ndimidzimu nakha amasowa chani kuti mpaka kukapanga chibwedzi ndi muthu wina,,,,,,,,

""Ndiye apa titani?
""uziti ndiye nditani osati titani ayi.
""Mesa unati undikwatira ndiye tiye undithandidze katundu tizipita kwanu?
"""Kkkkkkk kodi kwathu unayamba wabwerako, choti uziwe ine ndiri ndimkadzi moti abwera lero kuchokera kumudzi ndiye usazivutitse odi ndizipita ine.
"""Joe ndiweyo ukuyakhura zimenedzi zowoba?
""Ine ndimangofuna kuti ndizipedza popumira ndipo ndimasowa pokusira koma apa ndiye zatheka basi,,,,,,,Ngati masewera Joe ananyamuka kumapita kwawo kumusiya zimayi osakhutisidwayi manja alinkhutsi,,,,,,Apa sanachitire mwina koma kuyamba kulongedza akatundu awo kuyamba ulendo wobwelera kwamakoro awo,,,,,,,,,,

""Kumba za Ken ndiye anafika bwino kwambiri ndipo maphunziro anawayamba ndithu mwapamwamba komaso iye samalimbana ndi zamuthu moso ake anangoyika pamaphunziro basi, , ,,,,,,,,,,,,,,,,,,,,,By Kenneth

Pangani like page ino kuti nkhani zidzikupezani mosavuta,,,,,,,,,,

Osayiwara macoment chifukwa uku ndiye kudya kwanga......

24/08/2021

Hy guys, kaya mwadzuka bwanji? Ine ndadzuka bwino ndithu chabe ma busy. Ndafuna ndikuwudzeni kuti kwalero sizitheka mwina tiwone mawa kuti kubaranji. Koma osadera nkhawa chilichonse chiyamba kutheka bwimobwino......

20/08/2021

UMASIYE KUWAWA
😫😫😫😫😫😫😫😫😫😫😫😫😫😫😫😫😫😫😫😫😫😫😫😫
PART 7
mu part six tinasira pamene Ken akukozekera mayeso kuti ayambe pamene Mr Gama ntchito yawatheraπŸ‘‡πŸ‘‡πŸ‘‡πŸ‘‡πŸ‘‡πŸ‘‡πŸ‘‡πŸ‘‡πŸ‘‡πŸ‘‡πŸ‘‡πŸ‘‡πŸ‘‡πŸ‘‡πŸ‘‡πŸ‘‡πŸ‘‡πŸ‘‡πŸ‘‡πŸ‘‡πŸ‘‡πŸ‘‡πŸ‘‡πŸ‘‡
Hy hy!!, chukundichitikara ndichani ine zowana ntchito yandithera. Iyi ndiye timati minyama chifukwa muthune ndiye ntchito ndimagwira molimbika, koma kundichotsa mwachipogwe chonchi tiwonetsana,,,,,,Madara ine ndiye ndikufuna ndalamatu?"""Iwe chisiru eti osamapita kuschool uko bwanji.
""Komatu ndikupephani mwachulungamo, chifukwa sindikufuna kuti munditenge woyipa.
""Iwe usandidwalitse mutu, Choti uziwe pakharidwe lomwe unayamba sindingakupatse ndalama ungozitayitsa nthawi yako ,,,,,,,,Yobu anachoka koma mumtima mwake mukuwira ukari moti amangodikira Dara yakeyo ichoke kenako akayibere mix zibaba za chamba.,,,mosakhalitsa Mr Gama anasuthadi koma samadziwa kuti mwana wawoyi alikomweko ndipo akuwawelenga,,,,Atangochoka Yobu analowa nyumbamo ndikuyenda street kuchipinda kwamakoro akewo, Ndipo anayamba kuyang'ana mwamwayi anapedza mpukuta wandalama omwe Madara ake alandira kuntchito kwawo. Yobu sanachedwe koma kutapapo pafupifupi harf ndikunyamuka ulendo okasangalara........

"""Mayeso ndiye ndinawayamba bwino ndipo kwa ine chilichonse chinari nchimake,,,,,Ken mayeso wawawona bwanji?""Sam ndisanane ineyo ndiye andiphwekera kwambiri moti sindinawawone kuvuta kwambiri.
""Bora Amzathu koma ife ndiye eeee simene ativutira.""Vuto ndilakuti sumafuna kuwelenga ndiye unayiwalatso kuti class yomwe uliyo ndiysmayeso,,,,,Chomwe ungachite ukuyenera kusiya Kaye zibwana ndikuyamba kuwelenga kuti ma subject inawa asakuvute.,,,""Apadi ukunena zowona man chibwana chimalanda ndaziwa lero,,,,,Wawa gays?"""Wawa kodi ndi Moureen?
""Eya ndineyo ndithu.""Ok ndakulandira khara omasuka,,,,,Gays ine ndiye ndikuthawenitu?"""Mmmmm mukuchoka chifukwa choti ndabwera ine bwanji,,,Sam kuchokakutu anari manyadzi chifukwa Anakanidwa ndi njore yogometsa mafukoyu,,,,Mmmm ayi koma kungoti ndikufuna ndikawone ziwiri zitatu kuti mwina tikamakariwa kachiwiri ndisakavutike.""Ok man tiwonana,,,,,,,Sam anandisiya ine ndi Moureen,,,,Daer koma mayeso wawayamba bwanji?
""Ken ineyo kwa ine ndawayamba bwino kwambiri, Kaya iweyo honey?
""Ineso ndawayamba bwino ndipo sindikuwopa ayi,,,,,,Masiku ndiye amapita mpaka tsiku lomaridza mayeso linakwana ndipo siku limeneri ndilomwe linari gara,,,,,Honey apa sitikavinisana basi?""""Mmmm More inetu sinditha kuvina,,,Kkkkkk Ken mesa chilichonse ndikuphunzira basi, ndiye tiye ubwino wake ineso sinditha.""Ok tiye tikasangalare pakuti Mulungu watikomera kuti tilembe mayeso ndikumalidza."""Zowonadi Dear,,,,,Masiku ndiye amatha Ken akudikira matcheru kuti kugwanji, nawo Mr Miladzi amadikira kuti nwana wawoyi abweletsa zotani.

"""Mr Gama atabwera komwe analiko analowa nymba ngakhare analedzera koma amatha kuzindikira chomwe akuchita. Atafika nyumba anadabwa kuchipinda kwawo kuli puluru,,,,Aaaa inetu mene ndimachoko ndinaseka kuchipinda kwanga, Ooooh Yobu Yobu!! Ndalamazanga ine,,,,,,,Agama anapita pomwe anayika ndalama ndipomwe anazindikira kuti ndala zawo dzina zapita,,,,,,Oooh kana ndalama zanga amaba ndi ameneyi eti, Akanakhara kuti Ken alipo bwedzi zikuthera kwa iye,,, Ooh nchemwari ndikhulukire ndinathamangitsa magadzi anga.,,,
Kodi ndiye mukulira zichani apa?
""Garu wako waba ndalama zanga zomwe ziri ngati chipukuta misodzi.
""Mukutathaudza chani mukati garu wanga komaso chipukuta misodzi?
""Yobu waba ndalama zanga, komaso andichotsa ntchito.""Mukufuna kundiwudza kuti ntchito yatha?'""Ukufuna ndiyakhure bwanji? Komaso unandipangitsa ine kuti ndithamangitse magadzi anga, ndimawona ngati Ken ndiyemwe amaba pakhomo pano koma ndichimwana chako chomwe chimapanga zonsedzi.
""Kaya zanu idzo odi ndidutse ndikapume ndatopa.,,,Owowo zanga iti, zomwe zikusonyedza kuti sidzokukukhudza oro pang'ono?Tiwonesana ndipo ndikangomupedza ndimupanga zoti asadzandiyiware. Uyelekedze kumuvuladza mwana wanga uwonaso,,,,,,Mr Gama chithu China chinawadabwitsa maka kwa akadzi awo kamba zovara zomwe anavara sidzomwe avara pobwera komatso zinari zapamwamba,,,,,,china chake chikuchitika nyumba muno koma ndikukuwudza kuti ndikazangogwira sandizakhululuka ayi....

""Ken Ken sungakhulupilire?
""Chani uncle, Nakha kwagwanji?
""Iweyo ndimachine ndipo mwa iwe ndikondwera.""uncle tanenani mutiphatu ndi phuma?
""Wakhodza mayeso ako moti iweyo college yako ukukaphunzira kunja basi, Ndipo ino ndimthawi yoti ndikupatse Mphatso yako sopano chifukwa wachita chithu chomwe chinyawuditsa kwambiri,,,,,Ndinawona Uncle akundibwelesera suti yapamwamba kwambiri komaso sapato kundipatsa,,,,,Uncle ndikulephera kuthokodza kwake kuti ndingayambire pati, koma chomwe ndingakuwudze ndichakuti mphoto yomwe ndizakupatse izakhara yodura kwambiri ndipo ndikukulonjedza,,,,,Ki kiiiii!!!!! ooh Moureen ndakulandira?
""Zikomo chimphona changa chomwe chadodometsa mafuko chifikwa chakukhodza bwino.
""_Mmmmm kodi wadziwa kare eti?
""Eya moti kubwelaku ndimafuna zakutenge kwathu akukomzera mphatso yapadeledera.
""Zitheka bwanji?
""Usadabwe ndizakuti ndinawaudza kare za iwe moti kwangosara kuti akuwone live.
"""Oooh ok tiyeko bora tisakathilidwe nkhokotu kkkkk.
""Mmmm iwe tatiye ndipo I hope ukasangalara ndi mphotso imeneyi.

""Chisare koyamba ndikufuna ndipepetse kamba kosakumvera palangidzo ako, ndikukhulupilira kuti zonse zikuchitika panodzi chifukwa cha mwana uja ,,,,,,,,,,,,,Kodi zitha bwanji idzi. Pangani like page ino kuti nkhani zidzikupedzani mosavuta.

Oasayiwara mocoment anu ndiye kudya kwanga......................



BY KENNETH

19/08/2021

UMASIYE KUWAWA
PART 6
😫😫😫😫😫😫😫😫😫😫😫😫😫😫😫😫😫😫😫😫😫😫😫😫
Mu part five tinasira pamene chimzake cha Ken ndi Moureen chitafika pokomaπŸ‘‡πŸ‘‡πŸ‘‡πŸ‘‡πŸ‘‡πŸ‘‡πŸ‘‡πŸ‘‡πŸ‘‡πŸ‘‡πŸ‘‡πŸ‘‡πŸ‘‡πŸ‘‡πŸ‘‡πŸ‘‡πŸ‘‡πŸ‘‡
Idzitu zinapangitsa kuti Azikhodza kwambi chifukwa onsewo samapanga zachibwana, ngakhare Aphunzitse amachita kudxiwa kuti class mwawomu muri Ana achabe kwambiri."""Ken wawakonzekera bwanji mayeso?'"'Aaaa ndawakonzekera bwino kwambiri moti sindikuwopatso ngakhare pang'ono.
""Ok ineso sindikuwopa ayi moti uzidziwa kuti tipikitsana kwambiri.
""Kkkkk koma sikuti ungandipotsetu coz ine ndiye ndiwachabe.
""Mmmmm ok, koma iweyo ndimuthu wina wina wapadera.""Moureen ukufuna utathawudze kuti chani?'""Ndikufuna kutathawudza kuti akanakhara Amuna inawa bwedzi atandifhsira kare koma iwe suri choncho, chifukwa chani?
""Ukudziw chani more ineyo sikuti zolakorak sizindigwira ayi, koma ndimazibwedza and zimenedzo ndizapanga mwina ndikazalemba mayeso a form four.
""Iwe ndiye ulingati ineyo, koma palichimodzi chokha?
""Chani chimdnecho?
""Ineyo ndiye ndinagwa nawe mchikondi komano ndingofuna kuti uzidziwa ukazangolemba mayeso akowo usadzapite kwina coz ine ndakukonda?
""Mmmm ok ndakumva pepho lakoro, koma ngati ukufuna zimenedzo tidzichez ngati kare osati usithe zichitika chifukwa ndavomera zofuna zako ndiye uzanditenga ngati oyipa.
'""Ndakumvani, ubwino wake tonse chomwe tikufuna tikuchiziwa. Athuwa kuyambira tsiku limenero ndiye gwilidzo wawo unakura kopotsa moti athu ena amayesetsa kuti agwire nkadziyi koma iye amawakana mogometsa kumati ali kare ndimamuna ,,,,,,,,,Mayeso ndiye analembedwa moti chinasara kwa anawa ndikudikira zosatira basi.""phwanga chiyembekedzo chako chilipati maka za mayeso?
""Uncle inetu muziyembikedzera kuti ndipedzeka pa top.""Oooh ukangokhodza momwe ukunenera ndiyekuti ndikupangira chithu chapamwamba kwambiri.
""Zikoma kwambiri Unlce,,,,,,matsiku ndiye amapita ndipo mayeso anathuluka ndipo mwachiyembekedzo chomwe Ken anari nacho zinachitikadi chifukwa iyeyo ndiyemwe anari pa top. Kumbari ya Moureen naye anachita bwino kwambiri koma sanamupotse Ken,,,,,,

"""koma ndiye mchemwari wanga ndamusowa bwanji, ndipange bwanji kuti ndikumane naye,,,,,,Malume ndiye mwadekhati mukuganidza za Moureen kapena?
""Sam bwanji nthawi zonse umakamba nkhani zosephana?
""Sikuti ndizosephana komano ndikunena chulungamo.
""Ok koma ineyo ndiye sindikuganizo dzomwe ukunenadzo. Athawa anachedza nkhani zambiri mpaka kunja kunada,,,,,,,,,Masiku ndiye amapita ndipo Ken school ndiye imamuthekera kumbari inayi chikondi chake ndi Moureen moti atha ambiri anayamba kudziwa kuti ari Chikondi, moti pomwe pangapedzek Ken Moureen naye amapezeka pomwepo. koma ngakhare zinari chonchi prefornce yawo sinatsike anayi. Zomwe zimapangitsa kuti Aphunzitse asamalimbane nawo.

"""Kumbari ya Mr Gama ndiye ananamidzi ndi Akadzi awo kuti akupita kumaliro koma iyi inari plan yochokera kuti akanjoye ndi chibwedzi chawo, Moti zinatheka bwinobwino koma ngakhare amapita nkhawa anari nayobe maka kwa mwana wawo Moureen kuti sadzawaulura,,,,Honey mukuganidza chani?"""Mmmm iwe ndikuganidza za mwana uja anatiwona tsiku lijari kuti sakanena kwa Madara ake.
""Akanakhara kuti akufuna kuulura bwedzi ataulura kare, ndiye usadabdaure oro atakuthamangitsa ine ndiliokodzeka kukukwatira coz umandifikapo saname,,,,,,Idzitu zimachitika ari ku jonz pomwe uku Agama amangoti Madam awo ari kumaliro osadziwa kuti katundu akutha uku kkkkkkk.
""Agama mukuyitanidwa kuoffice.
""Ndalakwatso chani ine?"""Kaya ingopitani mukadzimvere nokha komweko,,,,Mr Gama anapitadi Ku office kuja komwe anapedza akuluakuru atakhara pamalopa,,, Mr m***a kukhara apa? Ooo zikomo kwambiri.
""Ife takuyitanani tafuna tikuwudzeni kuti malingana ndi zithu ziliri pano maka ndi covid 19 Taganidzi zochotsa athu ina ntchito, maka athu omwe samawonetsa chidwi ndiye mwamodzi wawo ndinuyo. Ndiye awa ndimalipiro anu komatso chipepetso chanu.
""Koma bwana inetu ndimalimbikira kwambiri nakha ndiye chifukwa chani?
""Mmmm ifetu tisanachotse mothu ntchito timayamba tawunika zambiri ndiye inuyo musatitayitse nthawi tingani ndalama zanu muzipita tikazakufunani tizakuyitanani.
Ngati bodzo Mr Gama anachosedwa ntchito ndipo chowo chinari chisoni, makatso akaganidzo zomwe akuchita akadzi awo komatso mwana wawo Yobu anabalarikiratu, Ichitu chinari chiyambi chamavuto kubanjari.

""Kukamba za Kenneth ndiye nyengo zake dzinari pabwino kwambi chifukwa amakhara bwino ndi Mr Miladzi, Panthawiyi nkuti akudikira mayeso a Four kuti alembe.,,,,,,,Ken ngati ukufuna kuti ukaphunzire Kunja ukuyenera kuchita bwino mayetso ako wandimva?
"""Ndakumvani ndipo ndilimbikira kwambiri kuti ndisakuchitiseni manyadzi.
""Ndimakukondire chokhacho,,,,, Tsiku lina Ken ari nkati mophunzira kunabwera Ahead omwe anabwera ndi uthenga omwe unamupangitsa Ken kuti alimbikire kwambiri,,,,,,Ndabwera ndi uthenga kwa inu oti yemwe angakhodze bwino Azakaphunzira kunja kwa dziko lino ndipo maphunziro amenewo azakhara aulere ndiye mulimbikire.,,,,,,,Ken wazimvera wekhatu?"""Yeah ndipo kwambiri, apa zikuwonetsa kuti tikhara pampikitsano kwambiri ndipo ndilimbikira kopotsa, paja pachichewa palimawu akuti kutchora mkhobwe ndima ndiye ndikuyenera kupanga kuthekera basi.
""Yeah zowonadi maka apa tangosara ndi mwedzi umodzi basi kuti tilembe,,,,,Kuyambira pomwe Ahead analengedza zokhudza kukaphunzira kunja Ken ndiye samachoka pamabukhu ndiye poti amakhara ndi Aphunzitsi momwemo ndiye kunari kuthandizana sizibwana, moti panalibetso kuchedza ayi,,,,,Tsiku ndiye linakwana loyamba mayeso kumbari ya Ken ndiye palibe chomwe amawopa mix anari atakodzekera kwambiri,,,,,,,,,,,,,,,, ,,, ,


BY KENNETH

Want your school to be the top-listed School/college in Nyambadwe?

Click here to claim your Sponsored Listing.

Location

Telephone

Address


Chilomon
Nyambadwe