Build Islamic Schools.

Build Islamic Schools.

Share

To establish facilities of learning, worship, and care such as centers, Mosques, Schools, universiti

27/10/2023

Registered organization.

Uwu ndi mgwirizano wa Asilamu m'Malawi muno kuti tikhale ndi zipatala zachisilamu komanso masukulu achisilamu kuyambira pulaimale mpaka kusekondale kuphatikiza univesite pogwilisira ntchito swadaqa yanga komanso swadaqa yanu.

Msilamu wina aliyense amene uthengawu ungamupeze akuyenera kutumiza kangachepe kena kalikonse kamene angakwanise malingana ndikupeza kwake.

Kumbukirani kuti ntchitoyi munthu mmodzi sangakwanise koma tonse tikuyenera kutenga nawo mbali.

Panopa tayambapo kale kumanga Build Islamic primary school ku Phalombe T/A Jenala tamanga block imodzi yomwe ili ndi zipinda ziwiri, standard 1 ndi standard 2, drag store and tuck shop, ku Phalombe T/A Jenala.

Apa tikutolera ma swadaqa omangila standard 3 ndi standard 4.

Aliyense akutumiza swadaqa yake kwa Msungi chuma wa Build Islamic schools, Shackra Sophia idrisah pogwilisira ntchito Mpamba, Airtel money, mukulu and Paisa pamanambala awa.👇👇
+265991852384
+265883781215
DZINA: Shackra Sophia idrisah

Inu amene uthengawu wakufikilani tumizilaninso ena

https://chat.whatsapp.com/DBKkEquoqQL27YSOm7TKNz

03/10/2023

Alhamudulillah

30/08/2023

Join us

18/11/2021
01/03/2021

KODI SADAQAH JARIYAH NDI CHANI?

Sadaqah Jariyah imatanthauza swadaqah yopitilira, yokhazikika komanso yosalekeza. Iyi ndi imodzi mwazinthu zabwino kwambiri zomwe tingachite m'miyoyo yathu monga kuchita ndikupereka mitindu imeneyi ya swadaqa.Titha kukolola m'moyo uno komanso moyo omwe uli mkuza

Ndime yochoka m'qur'aan: Suurat Yaa-sin (36:12)

إِنَّا نَحْنُ نُحْيِي الْمَوْتَىٰ وَنَكْتُبُ مَا قَدَّمُوا وَآثَارَهُمْ ۚ وَكُلَّ شَيْءٍ أَحْصَيْنَاهُ فِي إِمَامٍ مُّبِينٍ ﴿١٢﴾

12. Ndithu, lfe tidzaukitsa akufa, Ndipo tikulemba zimene atsogoza (M'dziko lapansi m'zochita zawo) Ndi zomwe amasiya pambuyo (atafa, Zonkerankera mtsogolo), ndipo Chinthu chilichonse tachilemba M'kaundula wopenyeka (wofotokoza Chilichonse).

___________________________________

Tipemphe Allah SWT atilipire tonsefe pazabwino zathu komanso zochita zathu za sadaqah,ndipo atipatse tonse malo ku Jannah. Ameen.

Chonde lingalirani zopereka sadaqa jariyah ku Build Islamic Schools Bungwe lomwe likumanga Masukulu ndi Zipatala zoyendera Sharia ku Malawi.

Pempho lathu la sadaqah jariyah tikufuna kuti tithandizire kupeza ndalama zomalizisira sukulu yomwe ili ku Phalombe yomwe chili chose chikuyenda koma pasala standard 6 mpaka standard 8.Ndi chithandizo chanu, titha kupitiliza kumanga sukuluyi komanso kufikira nsanga madera ena adziko la Malawi.

__________________________________

Ndime yochoka m'qur'aan: Suurat Al-Munaafiquun (63:10)

وَأَنفِقُوا مِن مَّا رَزَقْنَاكُم مِّن قَبْلِ أَن يَأْتِيَ أَحَدَكُمُ الْمَوْتُ فَيَقُولَ رَبِّ لَوْلَا أَخَّرْتَنِي إِلَىٰ أَجَلٍ قَرِيبٍ فَأَصَّدَّقَ وَأَكُن مِّنَ الصَّالِحِينَ ﴿١٠﴾

10. Perekani mwachangu (panjira ya Mulungu) zina mwa zomwe Takupatsani, isanamfikire mmodzi Wainu imfa (mwadzidzidzi) ndi Kuyamba kunena (modandaula), Mbuye wanga! Bwanji Osandichedwetsa nthawi pang'ono Kuti ndikhulupirire (ndi kuti ndikapereke swadaqa) ndi kutinso Ndikhale mwa anthu anu abwino.

وَمَا لَكُمْ أَلَّا تُنفِقُوا فِي سَبِيلِ اللَّهِ

(Al-Hadid)👆🏻👇🏼

10. Kodi ndichifukwa chiani Simukupereka panjira ya Mulungu (Chuma chanu) ?

...... أَلَمْ يَأْتِكُمْ نَذِيرٌ

(Al-Mulk)👆🏻👇🏼

8.Kodi sadakufikileni mchenjezi?


قَالُوا بَلَىٰ قَدْ جَاءَنَا نَذِيرٌ فَكَذَّبْنَا......

9. Adzayankha 'Inde, adatifika mchenjezi Koma tidatsutsa.......

___________________________________

Mukhoza kutumiza chopeleka chanu ku Build Islamic Schools kuzera pa Paisa,Mukuru komanso Airtel Money.

Tumizani chopeleka chanu kwa nsungi chuma wa Build Islamic School (Sister Shackira Sophia Idrissah) pa nambala iyi +265991852384.

Mukatero tumizani pa whatsapp message yanu ya umboni pa nambala iyi +260950312010

________________________________

Asilamu ambiri amasankha kupereka ndalama pomanga mzikiti kuti apeze mphotho zazikulu. Zofanana ndi izi, m***a kuthandizanso pomanga sukulu,chipatala kapena malo osungira ana amasiye.

Mphotho zanu zidzapitilira mpaka pa qiyama kamba kowolowa manja kwanu.

Muzalipidwa, Wodwala aliyense yemwe azathandizidwa muzipatala zimenezi komanso aliyense amene azaphuzira masukulu amenewa mphotho zake zizabwera ku account yanu.

Ndichinthu chamtengo wapatali cha sadaqah ngati imeneyi yomwe ingakhudze miyoyo ya anthu osawerengeka.

TUMIZANI KUMAGULUPU ENA IMENEYONSO NDI SWADAQA

Want your school to be the top-listed School/college in Phalombe?

Click here to claim your Sponsored Listing.

Location

Category

Telephone

Address


Phalombe TA JENALA
Phalombe
BOX51195