Lifuwu Rice Research Station

Lifuwu Rice Research Station

Share

Lifuwu Experiment Station conducts
research activities on rice breeding
and agronomy

19/06/2026

Winter rice farming preparations.
Inu mwagaula kale fada?
Osafooka
🌾🌾🌾

Photos from Lifuwu Rice Research Station's post 12/06/2026

Mwakoma Nonse, tikuthokozeni Chifukwa chotsatira mwachidwi ulangizi wa mbewu ya mpunga kuchokera kuno ku Lifuwu Rice Research Station. Tikukhulupilira ndithu kuti pang'ono panzake mukupindura . Tithokozenso chifukwa Cha mafunso anu omwe akupangitsa kuti nafe tiziyenda ndi nthawi komanso kuzamitsa kafufuku wathu.

lero tikambirana za mmene mungapangire ma nazare anu mwa ndondomeko ngati munsimu.

1. KUSANKHA MBEWU.

-sankhani mbewu yanu kuchokera ku matumba omwe munasunga ndipo munalemba dzina la mbewu
- onetsetsani kuti komwe mukukatenga mbewu matumba a mtundu Umodzi wa mbewu anali malo amodzi . Osatenga mbewu kumalo osungira mbewu komwe matumba a mitundu yambewu zosiyana siyana anaphatikizana kapena kuti anaikidwa mwa chinansanganya.Chotsani njere zonse zomwe zili mphwepwa ndi zosiyana mmaonedwe ndi njere zna za mtundu wa mbewu imodzi.
- Kumbukirani kuti mbewu yokwanira ma kilogiramu 40 imakwanira hectare imodzi pamene ma kilogiramu 16 imakwanira ekala imodzi.

MALO A NAZALE.

-Malo a nazale akhale a thya thya thya (flat) , osati pena kukwera pena kutsika . madzi amakhazikika ndi kulowa pansi mofanana pamalo otelewa.
-Malo a nazare akhale komwe ziweto sizimafika ngakhale usiku. Ngati muli ndi mantha kumbali ya ziweto , mangani mpanda kuzungulira malo a nazale
-Onetsetsani kuti Malo a nazale ndi ofikirika nthawi zonse komanso madzi amafika mosavuta kapena kuti kutenga madzi ndi pafupi.

KUKONZA NAZALE

-unjikani zinyalala pa malo anazale ndipo zikauma ziwotcheni . izi zimathandiza kuti njere za mbewu zomwe zikadali mu dothi zife . Udzu ndi mpunga ongomera okha umapsyeranso limodzi mukaotcha. Phulusa lomwe latsala mutaotcha zinyasi ndi manyowanso.

-musaiwale zida ngati khasu, chingwe/linya, tepi , ma peg zifunikira pa ntchitoyi

-Gaulani malo a nazale pafupifupi phanzi limodzi mozama kupita pansi.

-phwanyani mauma/ mabuma/ magulumwa onse kuti malo akhale ndi tizigulumwa ting'ono ting'ono tomwe sitingavute kusungunuka
-Lembani makulidwe wa bedi .
Bedi limodzi likhale ma mita khumi mu litali ndi mita imodzi mu lifupi.

-Mabedi pafupifupi makumi awiri( 20) ndi okwanira pa hekitala imodzi ndipo Mabedi pafupi fupi 8 ,(asanu ndi atatu ) ndi okwanira pa ekala imodzi.

kuchoka bed imodzi kufika bed lina zitalikirane pafupifupi phanzi limodzi( ma sentimita 30) pamene kukwera kwa bed limodzi kukhale theka la phanzi lanu ( ma sentimita 15).
-Ka njira komwe mwasiya pakati pa bedi ndi bedi kamathandizira poongolera madzi komanso kuyenda mosavuta mukamagwira ntchito ya pa nazale.

-Thirani madzi pa ma bedi any kuti pafewe koma ngati panali pofewa kale , chinyezi chinalipo ndikhale ndiye kuti madzi mudzathira mukaika mbewu.

KUIKA MBEWU PA NAZALE.

-Ikani mbewu mu ka bigili , mbale kapena saka ndikumwaza bwino bwino pa ma bedi anu. onetsetsani kuti mbewu siinathithikane malo amodzi pa bedi . pofuna kupewa kuthithikana kwa mbewu, mwazani ndi manja mbewu yokwanira ma kilogiramu awiri( 2 kgs) pa bed iliyonse.
-kwilirani mbewu ndi dothi lotsala popanga ma bedi , mbewu isamaonekere mukaikwilira koma ngati ikuonekera , phimbirani ma bed anu ndi udzu kuopetsa mbalame kuti zingatoretore.

-wazani madzi a mulingo wabwino mutakwilira mbewu yanu kapena mutaphimbira mbewu yanu

-osaiwala kumadzathilira pa nazale kuti chinyontho chisamasowe pa nazale mbewu imere ndi kutuluka bwino. Kuthilira madzi pa nazare kumathandizanso kusungunura michere ya mmanyowa ndi feteleza.

MBEWU YOKUNDIKA.

Ngati mukufuna mukufuna mukaike pa nazale mbewu ya chimera tsatirani izi.

-ikani mbewu yanu mu ndowa / magiri womwe muli madzi okwanira
mbewu mu ndowa/ bigiri ikhalemo ma ola 24(tsiku limodzi) ili mmadzi.
Chotsani mbewu yanu mu ndowa/ bigiri ndikuilowetsa mmasaka .
Tsekani kukamwa kwa masaka ndi chingwe/ linya.
-kumbani dzenje / mayenje akulu bwino malinga ndi muyeso wa mbewu yomwe mukufuna kukafesa.
ikani mbewu yomwe ili mu saka/ thumba ija mu dzenje munakumba lija ndikukwilira / kufotsera bwino bwino.
-pakatha masiku osachepera awiri( 48 hours) , kaichotseni mbewu pa dzenje mukapeza yaphulika phulika , yapanga chimera mizu

10/06/2026

Shout out to my newest followers! Excited to have you onboard! Patrick Steven, Jennipher Phirisagawa, Agie Mwase, Khefie Kwendakufa Banda, Chicco Nthali, Jimmy Chindindindi Luhanga, Dickson Chimwanga, Fabiano Blanzioh Josaya, Fredrick Bandawe, Fanuel Zigwa, Chisomo Mazengera, Pungulani Micheal James, Master Maliro, Ahmed Sudais James, Beatrice Mthunzi, Osward Gandigandi-phiri, Chikondi Samuel Kapito, Diana M. Chirwa, Alex Mpando, Tony Shaba, Richman Goliath, Mercy Danielz Bwanali, Chitsanzo Njombwa, Shadrec Chigwenembe, Chimwemwe Tebulo, Constance Musopole, Clement Malangwasila, Umar Maulidi, Ali Kumtenga, Chibongah Jnr, Archangel Munthali, Afinda Alfred Afinda, Harvey AliLeo Ndindi, Isaac Chirwa, Collings Batison, Prosper Idris Dada, Felix Chilomo, Spencer Matandala, Kenneth Chipeta, Phady Lozo, Chikondi Chanthunya, RÅ“ Se

Photos from Zodiak Online's post 06/06/2026

🌾🌾🌾🌾

05/06/2026

Moni Moni alimi a mbewu ya mpunga uko konse komwe muli.

Lero pa 5 mwezi wa June ife azilangizi anu a mbewu ya mpunga Kuno ku Lifuwu Research mogwirizana ndi nthambi yazakakufuku wa ulimi wosiyana siyana MMalawi muno( Department of Agricultural Research Services -DARS), tinali ndi chionetsero Cha mbewu ya mpunga. Chilinganizochi chinakonzedwa ndi thandizo la thambi yopititsa patsogolo mbewu zomwe zangotulutsidwa kumene kuti alimi apindule ( Agricultural Commercialization- AGCOM.

Chionetserochi chinabweretsa pamodzi alimi a mmasikimu ndi ma koparetivi monga Koperetivi ya Limphasa, koparetivi ya Lifuwu,koparetivi ya Mkondezi komanso bungwe la alimi loyendetsa madzi mu sikimu ya Lifuwu. Akulu akulu ena ku chionetserochi ndi monga adindo osiyanasiyana a ku unduna wa za ulimi ku likulu ku Lilongwe, adindo ku ofesi ya za ulimi ya Salima ( ADD ndi RDP), oyang'anira malo a za kafukufuku a Mkondezi, Lifuwu Baka ndi Kasinthula. Mulendo wathu wamkulu pa chionetserochi anali wamkulu wa nthambi ya zakafukufuku muno MMalawi Dr Grace Kaudzu.

Alimi anatenga magawo angapo kuphatikiza kulongosola mmene akupindulira ndi ndondomeko yolandira mbewu ku ofesi ya za kafukufuku komanso kuthandizira potulutsa mbewu yomwe alimi eni ake ayikonda

Akulu akulu pa kafukufuku wa mbewu ya mpunga analongosola ndi kuyankha mafunso a mmene mbewu za nyuwani zikuchitira mminda mwa alimi maka pa zokolora ndi masiku omwe mbewu zosiyana siyana zimatenga kuti ziche.

Alimi adzionera okha mbewu monga Nunkile, Wachangu, Mtupatupa, kudya, Makafaci , Linga, Mthetsanjala, Nazolo, Uwemi, Kilombero ndi Zina zambiri zomwe mungalime kuwiri pa chaka kupatula Kilombero ndi Faya

Zikomo

05/06/2026

Greetings from Lifuwu Rice Research.

Today , 5th June 2026,Lifuwu Rice Research in conjunction with the Department of Agricultural Research Services (DARS) organized a field day under Agricultural Commercialization program (AGCOM). The field day drew participants from Limphasa Rice Cooperative, Lifuwu Rice Cooperative, Lifuwu Water Users Association, Lifuwu Seed Growers Association, Officials from Salima Agricultural Development Program, Salima Rural Development Program, Baka , Mkondezi, and Kasinthula Research Station and Director of Agricultural Research Services Dr. Grace Kaudzu.

Farmers took turns explaining how they are benefiting from Research to Farmer Seed. diffusion programs and being part and parcel in Participatory Varietal Selection whilest appreciating variety crop stand

Scientists and technicians also answered questions from farmers and other officials on performance( yield and maturity period).

Amongst the varieties showcased include ,Nunkile ,Mpheta,Nanzolo, Kilombero,Faya 14 M69 Katete, Kayanjamalo,Wachangu Makafaci,Kudya,Linga,Mthetsanjala and Mtutapa. All of them except Kilombero and Faya 14 M69 can be grown both in Winter and Summer.

Regards.

28/05/2026

Mwakoma nonse alimi ambewu ya mpunga mmadera onse komwe tili. Potsatira kulengeza koyamba kwa nyengo ya mvula ya mchaka cha2026/27 muuthenga omwe a nthambi ya zanyengo anausindikiza pa tsamba la mchezo la wailesi ya Zodiac pa 24 May 2026 akuti mdziko muno titha kudzakhala ndi mvula yocheperako( El-Nino) chaka Cha ulimi chikubwerachi.

Pa chifukwa ichi, tachiona Cha nzeru kuti tikulimbikitseni za kufunika kwa ulimi wa mthilira mma sikimu ,mmadambo komanso mmalo ena omwe ulimi wa mthilira ( June-November) umatheka.
Tiyeni tipezerepo mwayi ochita ulimi wa mthilira kuti tiwonjezere zokolora ndikudzapanga phindu loonjezera pamwamba pokhala chakudya Cha pakhomo chokwnira ngakhale ng' amba itatikhudza

Zina mwa mbewu zovomerezeka zomwe mungalime nthawi ya ulimi wa mthilira ndi monga izi:

Mbewu. Masiku ochera Zokolora

Nunkile 112 5.4 tan/ hek

Kayanjamalo 110. 6.5 tan/hek

NERICA 4. 90. 4 tan/hek

Mtupatupa. 120. 6.3tan/hek

Katete. 94. 6 tan/ hek

Nazolo. 115. 7 tan/hek

Mpheta. 110. 7 tan/ hek

Mpatsa. 100. 5.8 tan/ hek

Makafaci 115 7 tan/ hek

Wachangu. 110 6.7 tan/hek

Mbewu zinanso ngati Kudya, Linga, Mtsetsanjala zomwe zangotuluka kumene zikupezeka ku office yathu pa mtengo wa K10, 000. pa kilogalamu.

Uthenga wa kuchepa kwa mvula mchaka chikubwerachi usatipangitse befu kapena kuti mpanipani chifukwa chakuti uwu ndi mwai wathu owonjezera zokolora ngati titagwilitsa ntchito mwai wa ulimi wa mthilira ukubwelawu.

Zikomo.

28/05/2026

Greetings from Lifuwu Rice Research Station, your ally in rice. A pre-liminary weather forecast from the Department of Meteological Services delivered through Zodiac Broadcasting Station on 24th May 2026 suggests that Malawi will experience El-Nino( below normal rains) during 2026/27 rain season

With that in mind, we would like to encourage rice farmers to utilize winter season ( June-November) to grow rice in schemes, dambos and all the irrigable areas.

Basic seed of different rice varieties for winter rice cultivation is available here at Lifuwu Rice Research at K10 000 per kilogram with details below,

Nunkile 112 days 5.4 ton/ ha

Kayanjamalo 110days 6.5 ton/h

NERICA 4. 90 days 4ton/ha

Mtupatupa. 120 days 6.0 ton/ha

Katete. 94 days 6 ton/ha

Mpatsa 100 days 5.8 ton/ ha

Mpheta 110 days 7 ton/ha

Nazolo. 115 days 7ton / ha

Makafaci. 115days. 7 ton /ha

Wachangu 105 days 6.7tons /ha

The preliminary weather forecast should not cause panic but rather serve as a wake up call to explore initiatives to increase yield by taking an advantage of this coming winter season

Regards.

19/05/2026

Moni moni alimi anzathu a mbewu ya mpunga konse komwe muli. Ife alangizi anu tafika ndi uthenga ofunika kwambiri pankhani ya kakoloredwe ka mpunga, ena munayambapo kale ndipo ena mukufuna muyambepo kandimvelele anakanena za mmaluwa komanso paja amati kanalowa mkhutu kanayala mphasa

1. ZIZINDIKIRO ZAKUTI MPUNGA WANU WACHA.

- Masache/ ngala, njere zimaoneka mwa khakho( straw color) maka mpunga ngati Kilombero, Nunkile Mtupatupa ndi mitundu ina pamene Faya ndi NERICA 4 masache/ ngala zawo zimakhala za chikasu( golden brown

- Mapesi ndi masamba a mpunga nazonso zimaoneka za khakhi.

- Masache ( panicles ) amaloza pansi ( drooping).

- Nthawi zina mapesi ampunga amagwa / kugwera pansi chifukwa cholomedwa ndi kulemera kwa masache.

2. ZOTI TICHICHITE TISANAKOLORE.

a. Chotsani madzi mmunda wa mpunga masabata awiri kapena atatu musanapite kokakolora.

b. Chotsani madzeradzera (off types) ndi milakale/ chingwindimba ( mutants/ remnants ) yonse kuti masache ake asaphatizizane ndi mpunga.

Madzeradzera ndi chingwindimba / lingwindimba ndi zoipa mu mpunga
Chifukwa

-Mpunga wokhala ndi chingwindimba/ madzera dzera umakhala ndi timibulu takuda tomwe timakhala ngati mwatafuna mwala mu mpunga ndipo mpungawo sukoma.

- Madzeradzera/ lingwindimba amapangitsa kuti mpunga wanu olephere mayeso a mbewu ngati ndinu mulimi wa mbewu ( seed glower).

-Madzeradzera / lingwindimba zimakhala ndi njere za timinga kutsogoloku. zitha kukulasani mmaso.

3. ZIDA ZOGWIRITSA NTCHITO POLOLORA.

- Zisikiro, nangwape, makwakwa/ zikwakwa zogwetsera mapesi

- Ma Lora,(taupoline/ plastic sheet), zitanga, mikeka , poombera mpunga.

- Ukonje,lukonje,linja, zingwe, zosokera matumba
masaka,ndowa,mitanga ,zonyamulira mpunga

Zisongole. Ndunji zosokera matumba

Zolembera/ ma pental markers. Zolembera mtundu wa mpunga pa saka.

Malichero/ malisero. Zopetera mpunga kuchotsa mphwepmpwa

4. ZOCHITIKA POKOLORA.

Gwirani mphesi za mpunga zokwanira mchikhatho chanu( zokwanira mdzanja lanu) kenako dulani / gwetsani mphesizi ndi zikwakwa/ Zisikiro.

Unjikani mapesi omwe magwetsa kale mmiru yosavuta kunyamula pokasiya pa chitanga/ plastic sheet.

Ikani mapesi a mpunga mozungulira chilona/ chitanga ndipo masache onse ayang'ane mbali imodzi mozungulira lona yanu.

Ngati mwakwanitsa kuunjika mulu Umodzi mozungulira chilona Chanu ndipo masache ampunga ayang'ana mbali imodzi mkati mwa chilona yambani kuomba mapesi a mpunga kumenyetsa ku masache anzawo.

Mapesi onse omwe masache onse njere zagwera poombera mapesi amenewo atayidwe

Uluzani mpunga wonse womwe wagwera poombera kuti muchotse mphwepmpwa. Kuuluza mkumatheka bwino ngati kukuomba ka mphepo. Nyamulani mpunga mu lisero ndikuchita ngati mukuutaya pansi poombera , kenako kupani mpunga womwe wagwera poombera kumalizitsa kuchotsa mphwepwa.

Chenjezo.

Ngati mpunga wanu mwagwetsa lero ndibwino kuomba tsiku lomwelo chifukwa umagona musanaombe m***a kuberedwa ndi anthu achiipongwe usiku komanso mvula itha kubwera usiku ndikunyowetsa mpunga wanu. Mpunga wonyowedwa ndi mvula umakaduka kwambiri ku chigayo.

Mukamaliza kuomba, ikani mmasaka a nyuwani, sokani bwino bwino , ndikulemba mtundu wa mpunga pa thumba.

Want your school to be the top-listed School/college in Salima?

Click here to claim your Sponsored Listing.

Location

Telephone

Address


Lifuwu Research Station , P. O. Box 102
Salima

Opening Hours

Monday 07:30 - 17:00
Tuesday 07:30 - 17:00
Wednesday 07:30 - 17:00
Thursday 07:30 - 17:00
Friday 07:30 - 17:00