Latest from Edmond Bitoni

Latest from Edmond Bitoni

Share

POEMS FROM THE WORLD OF POETRY

14/04/2022

Pa chipatala chathu cha Thyolo pali vuto lalikulu la ukhondo.

Izi ndi kamba kakuonongeka kwa ma flashing toilets, vuto la madzi a water board.

Mwachitsanzo, ward imodzi yomwe mumakhala odwala opitilira 30, imagwiritsa ntchito toilet Imodzi yomwenso ndi yoonongeka.

Munthu akagwiritsa ntchito toilet yi akuyenera atunge madzi akathire kuti zoipazo zipite pansi.

Zaonetsa kuti vutoli ndi la pa ka nthawi.

Koma nanga adindo akutiponji?

04/04/2021

NO SABOTAGE

100% ndikugwirizana nazo izi, nanenso zimandidabwisa ndithu kuti kodi sukuluyi anawa akuyiyendetsa bwanji???😣😣

Nanga makolo mukulekelera ana pa maphunziro, akalephera kumaloza chala aphunzitsi, ayi sizoona.

Mwana wina aliyense wa sukulu, kaa ukuziona kukula, ndiwe mwana wa sukulu basi mvera aphunzitsi ndipo uzichepese. Ngati sutelo kuchita bwino pa maphunziro kuvuta.

Iweyo ukupita ku sukulu ndiwe candidate chotengeranso Bluetooth ndi chani? Foni mkati, MANEB kuyesa mzako?

Lero waumbuza 40 points, ena kusenza mgolo kumene ndie chodandaula nd chani??? Chonsecho ukudziwa kuti umakhalira mma birthday, mowa, fodya mkati, Ndakwiya.

Ndikati ndikuuze mafoni analiko, koma sitnapange umu muchitiramu. Ndiwe candidate koma ukukhalira usana/usiku wonse Facebook, whatssap.

Malo moti waweluka zipita kunyumba ukadye, ukapedze nthawi yowerenga, ndipamene uliyaviyavi ndi m'nyamata/mtsikana zithandiza???

Ati Zibwenzi? Zibwenzi zake ziti zoyambira ku secondary kapena ku primary? Ati vis is Richard my beft friend. Owo Friend? Menemo sukudziwa kuti iye kwawo akafika amatani, ma results kubwera iye waoloka iwe wagweramo. Musinthe.

Kumakhala ma discussion. Inde kuthandizana zinthu anyamata ndi atsikana pokonzekera mayeso, lero ma discussion ake ndi afeki; mupeza ma hours ochuluka akukambirana nkhani zosagwirizana ndi sukulu.

M'mutumo m'malo moyikamo zolongosoka, za sukulu, basi busy zinthu zolaula, mayeso abwera empty brain.

Ineyo ndinauzidwa mawu kamodzi ndipo ndinagwira mawu. Zilinso kwa iwe kuwagwira kapena ayi:

MANKHWALA A MAYESO NDI KUWERENGA 🙌

01/04/2021

APA NDI PAMENE TINGAZAZINDIKIRE KUTI KUUMBUZA 40 POINTS NDI CHAMUNA CHOMWE

06/08/2020

KATATU KA BUKU LOYERA
Katatu ka buku loyera kandidabwitsa
Azondi atatu adazonda sodomu ndi gomora
Eliya adapemphera, ndipo kudakhala chilala
Zilumika makumi atatu mkusiyapo theka
Katatu ka buku loyera kandibwitsa

Mose atabzalachinangwa,
A Israel anabuma maliro masiku atatu
Daniel Atatulukira upo wawo ku babulo,
Adanjunga kwa Yehova katatu pa tsiku
Kwa masikunso makumi atatu
Kupempherela za chinthuchi
Kodi amuna achikhulupirilo aja
Okana kulanbira fano la mfumu,
Sadali atatu?
Shadreck, Misheck, Abedinego
Inetu katatu ka buku loyera kandibwitsa

Photos 10/03/2020

Day 10 of our Recording Women Poets Celebrations sees us celebrate the life and work of Mercy Mbeta. Relatively new on the scene, Mercy has already released a number of local language poems that show that with consistency and time, she will curve her position amongst the best. We celebrate her life.

Download her poem, Mudakhala bwanji amuna by using the following link

https://sapitwapoetry.com/mercy-mbeta/3046/mudakhala-bwanji-amuna/

07/02/2020

BWENZI LA KU MTIMA
Ndalipeza langa bwenzi la Ku mtima
Bwenzi londigudulira chikondi mosasinila
Bwenzi lopanda banga
Bwenzi losatopa, inde lopanda nsanje
Bwenzi la Ku mtima
Mwa iye chinyengo mulibe
Bwenzi lokoma mtima,
Nlofafaniza tchimo la dziko la pansi
Ndikupereka wosatha moyo
Bwenzi la ku mtima
Ndi mchilikizo weni weni wa moyo wanga
Bwenzi losandi inga
Pa msautso, pa mtendere, tikhala nganga
Anga chitseko mferemu
Bwenzi losakhumudwisa
Pakuomba namondwe anditeteza
Ndikatelereka andigwira dzanja
Bwenzi la ku mtima
Lotaya wake moyo,
Pokhetsa mwazi pa calvary paja
Chifukwa cha wanga moyowu
Paja pa Gologota,
Pofunitsitsa kuti ndikhale mfupi naye
Dziko pokana kuunika, potsata mdima
Inde lindikonzera malo m'mwamba
Bwenzi la ku mtima
Langa thandizo lopezekelatu
N'kamva njala, andininkha mkate
Mkate wa wamoyo
Ndikamva ludzu, andikonkha madzi kukhosi
Madzi ondininkha moyo
Aja adamulonjeza namwali wa ku Samaria
Pa chitsime pajaaa
Bwenzi la ku mtima
Mpulumutsi wolonjezedwa, mau ofuula nchipululu
Kalonga wa mtendere,
Mfumu ya mafumu
Mamuna wantanda wa moyo
Woyesedwa katatu ndi mdielekezi,
Wogonjetsa imfa masiku atatu
Mchilisi wanga Ndikamva litsipa
Andipyoletsa mu nthunzi wa imfa
Inde andimenyera nkhondo,
Nalesa namondwe powomba
Bwenzi la ku mtima
Ndie mukandipenya kudekhaku,
Chimwemwe chodzadza sayachi,
Makolasi pakamwapa,
Bayibulo kudzanjaku,
Ndakatuloyinso iyi,
Dziwani Ndalipeza langa.
BWENZI LA KU MTIMA

02/06/2019
Want your school to be the top-listed School/college in Thyolo?

Click here to claim your Sponsored Listing.

Location

Website

Address


Thyolo